Zaka 7 kundende atamenya wangongole
Abambo asanu ndi m'modzi (6) munzinda wa Mzuzu, awagamula kukaseweza jere zaka zisanu ndi ziwiri (7) aliyese kaamba komenya munthu yemwe anakanika kubweza ngongole. Malinga ndi m'neneri wa apolisi mchigawo cha kumpoto Inspector Cecilia Mfune, anthuwa ndi a Atupele Khoma (34), Dumisani Kaunda (29), Jack Tambala (37), Lumbani Mbewe (26), Esau Kumwenda (34) ndi Charles...
bambo asanu ndi m’modzi (6) munzinda wa Mzuzu, awagamula kukaseweza jere zaka zisanu ndi ziwiri (7) aliyese kaamba komenya munthu yemwe anakanika kubweza ngongole.
Malinga ndi m’neneri wa apolisi mchigawo cha kumpoto Inspector Cecilia Mfune, anthuwa ndi a Atupele Khoma (34), Dumisani Kaunda (29), Jack Tambala (37), Lumbani Mbewe (26), Esau Kumwenda (34) ndi Charles Chamdothi (23).
Bwalo la Chief Resident Magistrate ku Mzuzu linapeza anthuwa olakwa pa mlandu ozembetsa, kusunga mokakamiza, kuthira madzi owononga thupi ndi kumenya a Kondwani Jere, atalephera kubweza ngongole.
Mfune wati, anthuwa anapalamula mlanduwu usiku wa pa 9 January 2026 mdera la Chiputula munzinda wa Mzuzu.
Iwo ati mboni ya boma inauza bwaloli kuti m’mwezi wa December 2025, a Jere omwe ndi namwino ku chipatala cha St Johns anakongola ndalama yokwana K11,800,000 ya bizinesi kuchoka kwa Dumisani Kaunda yemwe anali wogwira ntchito ku banki ya FDH ku Chitipa.
Iye anati usiku wa tsikuli anthuwa anatengera Jere m’chinyumba china chosamaliza kumanga mdera la Chiputula komwe anamusunga mokakamiza, kumumenya komanso kumuthira madzi omwe anali ndi mankhwara omwe anawonga thupi lake atazindikira kuti analibe ndalamayi.
Pa chifukwa ichi bwaloli linati anthuwa anachitira Jere nkhanza choncho akuyenera aliyese kukakhala kundende zaka zisanu ndi ziwiri aliyese.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.