Skip to content

Batchala wogwiririra mabuthu awiri akaseweza jere

Bwalo la mirandu la Salima First Grade Magistrate lagamula bambo wazaka 35 kuti akaseweze jere kwa zaka khumi ndi ziwiri (12) atapezeka olakwa pa mlandu ogwiririra mabuthu awiri a zaka 12 aliyese.Malingana ndi wachiwiri kwa mneneri wa apolisi m’bomali, Constable Veronica Kamphafa, bamboyu yemwe dzina lake ndi Samson Katema adachita izi m'mwezi wa May m'mudzi...

Malawi24
Jul 21, 20261 min read

walo la mirandu la Salima First Grade Magistrate lagamula bambo wazaka 35 kuti akaseweze jere kwa zaka khumi ndi ziwiri (12) atapezeka olakwa pa mlandu ogwiririra mabuthu awiri a zaka 12 aliyese.

Malingana ndi wachiwiri kwa mneneri wa apolisi m’bomali, Constable Veronica Kamphafa, bamboyu yemwe dzina lake ndi Samson Katema adachita izi m’mwezi wa May m’mudzi mwa Namwera kwa mfumu yayikulu Maganga.

Kamphafa wati woyimirira boma pa mlanduwu, Sub Inspector Winfred Mawindo adauza bwaloli kuti Katema ankaitana ana awiriwa kunyumba kwake komwe amakagonana nawo ndikuwapatsa ndalama ngati chitseka pa kamwa.

Koma tsiku la fote litakwana, Katema adagwidwa ndipo zotsatira za kuchipatala chachikulu cha boma la Salima zidatsimikiza kuti anawa adagwiriridwadi.

Poonekera ku bwalo la milandu, Katema anavomereza kuti ndi olakwa.

Pofuna kuti amupatseko chilango chochepekerako, iye adauza bwaloli kuti anawa amapita kunyumba kwakeko mwa okha komwe amakamukopa poti iye sanali okwatira.

Apa Sub Inspector Mawindo anapempha boma kuti lipereke chirango chokhwima kwa Katema ponena kuti zomwe anachitazi zisiya zipsera zazikulu mitima ya anawa mpaka moyo wawo onse.

Apa, First Grade Magistrate Amran Phiri anagwilizana ndipempholi ndikulamula Katema kuti akakhale ku ndende kwa miyezi 72 pa mlandu oyamba, komanso ina 72 pa malandu wachiwiri, zomwe zikutanthauza kuti akakhala kundende zaka 12.

Katema amachokera m’mudzi mwa Namwera kwa mfumu yayikulu Maganga ku Salima komweko.

Did you enjoy this article?

Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.

Across the AtmosphereDiscussions