Osewera amakhala ngati akulemedwa – Munthali
Wothandizira kuphunzitsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali wati osewera ake amakhala ngati akukakamizidwa pomwe agonja ndi Goshen City Dedza Dynamos.Marco Chiwaya anagoletsera Dedza Dynamos mu mphindu 40, kuti masewerowa athere 1-0.Atatha masewero pa bwalo la Dedza, Munthali anawuza olemba nkhani kuti FCB Nyasa Big Bullets sinasewere mmene amayembekezera."Mamenyedwe ake timakhala ngati timakakamizidwa"...
othandizira kuphunzitsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali wati osewera ake amakhala ngati akukakamizidwa pomwe agonja ndi Goshen City Dedza Dynamos.
Marco Chiwaya anagoletsera Dedza Dynamos mu mphindu 40, kuti masewerowa athere 1-0.
Atatha masewero pa bwalo la Dedza, Munthali anawuza olemba nkhani kuti FCB Nyasa Big Bullets sinasewere mmene amayembekezera.
“Mamenyedwe ake timakhala ngati timakakamizidwa” anatero Munthali atafusidwa kuti timu yake sinasewere bwino chifukwa chani. “Osewera amakhala ngati akulemedwa”.
Munthali anatiso timu yake inalephera kumenyera pagolo chifukwa choti imamenya mopanda cholinga pomwe inakanika kupeza mipata yokwanira.
Iye anati kugonja ndi Dedza Dynamos ndi chinthu chopweteka ndipo anapempha osewera ake kuti adziganizire pa zomwe zachitikazi.
Zotsatirazi zapangitsa Bullets kuti igwe kuchoka pa nambala yachitatu pomwe pano ndiyachinayi pomwe ili ndi mapoint 20 pamasewero 11.
Kumbali yake mmodzi mwa a phunzitsi a Dedza Dynamos, Luka Milanzi wati ndiwokondwa kamba ka chipambanochi ndipo anati akuwona timu yake ikumaliza mkatikati mwa ma timu khumi chikamatha chigawo choyamba.
Dedza ili pa nambala 13 itapeza ma point 11 pamasewero 11.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.