Skip to content

A Mutharika ali kuti?

Pomwe mphekesera zikuti a Mutharika apita m'dziko la South Africa, boma silinabwere poyera kufotokoza

Malawi24
Aug 5, 20261 min read

oma silikubwerabe poyera kufotokoza komwe kuli mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pambuyo pa mphekesera zoti wapita kunja kwa dziko lino.

Lachiwiri, wailesi ya boma ya Malawi Broadcasting Corporation kudzera pa tsamba lake la fesibuku, MBC Digital idalengeza kuti a Mutharika akupita m’dziko la South Africa paulendo osakhudzana ndi boma.

MBC idati a Mutharika amayembekezeka kunyamuka ulendowu masana a Lachiwiri kudzera pa bwalo la Kamuzu International munzinda wa Lilongwe.

Koma posakhalitsa, wailesi yabomayi, idafufuta nkhaniyi.

Nayo wailesi ya Zodiak Lachitatu lomwelo idatulutsa nkhani kuti a Mutharika atuluka m’dziko muno kupita kunja koma mwa chinsinsi.

Koma posakhalitsa, nayo wailesi ya Zodiak idafufuta nkhaniyi. Kupatula kufufuta nkhaniyi, Zodiak Lachitatu m’mawa yatulutsa kalata yopepesa mokhudzana ndi nkhani yomwe inatulutsayi.

Kudzera mkalata yake, Zodiak yati zomwe inalembazi linali bodza lankunkhuniza.

Ngakhale zili choncho, boma silinabwerebe poyera kufotokoza ngati a Mutharika ali m’dziko muno kapena ngati atuluka monga momwe mphekesera zikuvekeramu.

Nthawi zonse a Mutharika akamatuluka m’dziko muno paulendo wa boma kapena wawo wawo, mlembi wa mkulu wa boma amatulutsa kalata yofotokoza za ulendowo.

Did you enjoy this article?

Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.

Across the AtmosphereDiscussions