Skip to content

Ophunzira ku UNIMA wapha bwenzi lake lakale

Ophunzira yemwe wangomaliza maphunziro ake ku University ya Malawi (UNIMA) ku Zomba, wapha bwenzi lake lakale pomubaya ndi mpeni kwa Chikanda mu mzindawu.Malingana ndi wachiwiri kwa wofalitsa nkhani pa polisi ya Zomba, Andrew Mwale, mnyamatayu ndi Raphael Kenala Liko yemwe akuganiziridwa kuti wapha Shingirai Mbenje wazaka 17.Malipoti omwe tapeza akusonyeza kuti lachiwiri sabata ino, Shingirai...

Malawi24
Aug 5, 20261 min read

phunzira yemwe wangomaliza maphunziro ake ku University ya Malawi (UNIMA) ku Zomba, wapha bwenzi lake lakale pomubaya ndi mpeni kwa Chikanda mu mzindawu.

Malingana ndi wachiwiri kwa wofalitsa nkhani pa polisi ya Zomba, Andrew Mwale, mnyamatayu ndi Raphael Kenala Liko yemwe akuganiziridwa kuti wapha Shingirai Mbenje wazaka 17.

Malipoti omwe tapeza akusonyeza kuti lachiwiri sabata ino, Shingirai pamodzi ndi mzake wina, amachokera mtauni ya mzindawu komwe mayi ake amagulitsa malonda.

Malipoti akuti atayandikila kufika pa malo ena otchedwa pa Tholo, Shingirai anadabwa kuwona Kenala Liko yemwe anasiyana naye chibwenzi pa kanthawi akumudikira.

Atakumanizana, Kenala Liko anauza malemuyu kuti ayendere limodzi poti anali ndi zoti akambirane naye zomwe Mbenje anakana.

Izi zinakwiyitsa mnyamatayu yemwe anayambe kumumenya mtsikanayu, mpaka kutulutsa mpeni ndikumubaya pa chifuwa kangapo.

Pakadali pano,male watsimikiza kuti Kenaka Lino ali m’manja mwa apolisi pomwe akuyembekezeka kukayankha mlandu wakupha munthu.

Did you enjoy this article?

Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.

Across the AtmosphereDiscussions