Kuphunzira Galimoto kwaphetsa mwana ku Mangochi
Apolisi ku Mangochi amanga banja lina poliganizila kuti lagunda ndikupha mwana wazaka 8 pomwe anali kuphunzitsana kuyendetsa galimoto.Oganiziridwawa ndi Sande James azaka 51, wa m'mudzi wa Changamile 1, ndi Zainab Alli Mposa wazaka 40, wa m'mudzi wa Bulayima ndipo onse ndi a m’dera la mfumu yaikulu Chimwala m’boma la Mangochi.Malingana ndi apolisi, ngoziyi inachitika madzulo...
polisi ku Mangochi amanga banja lina poliganizila kuti lagunda ndikupha mwana wazaka 8 pomwe anali kuphunzitsana kuyendetsa galimoto.
Oganiziridwawa ndi Sande James azaka 51, wa m’mudzi wa Changamile 1, ndi Zainab Alli Mposa wazaka 40, wa m’mudzi wa Bulayima ndipo onse ndi a m’dera la mfumu yaikulu Chimwala m’boma la Mangochi.
Malingana ndi apolisi, ngoziyi inachitika madzulo a Lamlungu, pa 9 August 2026, m’msewu wadothi ku mudzi wa Changamile 1.
Apolisi ati James anali kuphunzitsa mkazi wake kuyendetsa galimoto yawo yamtundu wa Honda Fit, yomwe nambala yake ndi MH 1100A.
Pamene ankadutsa pafupi ndi nyumba ya m’nansi wawo, Mposa yemwe alibe laisensi yoyendetsela anataya ulamuliro chifukwa chothamanga kwambiri.
Galimotoyo inagunda Mariam Salade, wazaka 8, yemwe anali kusewera ndi anzake ndipo anapanikizika pa khoma la nyumba.
Mwanayo anavulala kwambiri kumutu ndipo anapita naye kuchipatala cha Boma la Mangochi, komwe anafika atamwalira.
Pambuyo pa ngozi banjali linathawa ndipo pambuyo pake James anapita ku polisi kukanena kuti iye ndiye anali kuyendetsa.
Komabe kafukufuku wotsatira anaonetsa kuti bamboyu anali kubisa mkazi wake, zomwe zapangitsa kuti onse awiri amangidwe.
Mposa akuyembekezera kuyankha milandu ya kupha munthu chifukwa choyendetsa mosasamala komanso kuyendetsa popanda laisensi.
James adzayankha mlandu wophunzitsa anthu kuyendetsa galimoto popanda kulembetsa.
Apolisi apempha anthu kuti asiye kuphunzitsa ena kuyendetsa galimoto ngati sanalembetse, chifukwa izi zitha kuyambitsa ngozi komanso kutaya miyoyo.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.