Skip to content

Masewero m’sukulu, gwero la Scorchers

Pomwe atsikana a Scorchers ku mpikisano wa WAFCON ku Morocco akudoda chikopa mopatsa kaso ngati si aku Malawi konkuno, zadziwika kuti ambiri mwa iwo lunso lawo linatumphuka kudzera m’mipikisano ya masewero m'sukulu.Mtsogoleri wazamasewero m’sukulu m’dziko muno, Blackson Malamula, wati 90% ya asungwana okankha chikopa ku timu ya dziko lino ya Scorchers, akuchokera kumipikisano ya m’sukulu...

Malawi24
Aug 12, 20262 min read

omwe atsikana a Scorchers ku mpikisano wa WAFCON ku Morocco akudoda chikopa mopatsa kaso ngati si aku Malawi konkuno, zadziwika kuti ambiri mwa iwo lunso lawo linatumphuka kudzera m’mipikisano ya masewero m’sukulu.

Mtsogoleri wazamasewero m’sukulu m’dziko muno, Blackson Malamula, wati 90% ya asungwana okankha chikopa ku timu ya dziko lino ya Scorchers, akuchokera kumipikisano ya m’sukulu m’dziko muno.

Malamula wati ngakhale zipatso siziwoneka pa nthawi yomweyo koma pakadutsa dzaka ndipomwe ambiri omwe anatengapo gawo mu mipikisano ya m’sukulu imawonekera.

“Temwa Chawinga anasewera Airtel Rising Stars mu 2012, ngakhale achina Madina Nguluwe anatenga nawo gawo mipikisano ya m’sukulu. Moti 90 peresenti ya atsikana omwe ali ku Morocco anachokera m’mipikisano yathu,” watelo Malamula.

Malamula amayankhula izi patsogolo pa mpikisano wa Malawi Youth Games wa chaka chachisanu ndichimodzi, omwe zigawo zamaphunziro zimapikisana pofuna kupeza katswiri wa dziko lonse.

Malamula: Masewero m’sukulu apindulira Scorchers

Chaka chino mpikisanowu uchitikira kumabwalo a Bingu, Civo, Kamuzu Institute komaso Lilongwe Community ndipo uchitika m’magawo a Mpira wamiyendo wa atsikana ndi anyamata, mpira wamanja, Chess, Basketball, Volleyball komaso Athletics.

Malamula wati kuchoka mu April pomwe mpikisano wa chaka chino unayamba, kwakhala kukutuluka luso lapamwamba ndipo wati akuyembekezaso kuti mpikisano wa chaka chino utulutsa lunso loposa zaka zonse.

Iwo ati pakadali pano zokonzekera za ndime yotsiriza ya chaka chino zatha ndipo ma timu anyamuka Lachitatu kulowera mu mzinda wa Lilongwe komwe kuli ntchito yonse.

Mneneri wa bungwe loyang’anira masewero onse mdziko muno, la National Council of Sports, Edger Mtulumbwa wati ndiwokondwa kuti ndalama zomwe akhala akuthandizira mpikisanowu kuchoka chaka cha 2021 zayamba kuwonetsa zipatso.

Mtulumbwa adakambapo za osewera ena omwe ali mu timu ya Scorchers omwe akuchokera ku mpikisanowu komaso akatswiri ena omwe anayimira dziko lino ku Region 5 komaso ku mpikisano wa Commonwealth.

Did you enjoy this article?

Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.

Across the AtmosphereDiscussions