Skip to content

Zonyera Zambuzi alongedwa kukhala Senior Chief Kachindamoto VIII

A Enoch Zonyera Zambuzi Kalapino azaka 61, awalonga ufumu kukhala Senior Chief Kachindamoto VIII, ndipo alowa m'malo mwa malemu Senior Chief Theresa Chidyaonga Kachindamoto VII, m'boma la Dedza.Mwambowu unachitikira pa bwalo la zamasewero la Dedza, m'bomali ndipo ufumu wa Kachindamoto wakhala opanda munthu kuchokera chaka chatha pomwe malemuwa adalowa m'manda.A Zonyera Zambuzi awalonga ufumu kutsatira...

Malawi24
Aug 12, 20261 min read

Enoch Zonyera Zambuzi Kalapino azaka 61, awalonga ufumu kukhala Senior Chief Kachindamoto VIII, ndipo alowa m’malo mwa malemu Senior Chief Theresa Chidyaonga Kachindamoto VII, m’boma la Dedza.

Mwambowu unachitikira pa bwalo la zamasewero la Dedza, m’bomali ndipo ufumu wa Kachindamoto wakhala opanda munthu kuchokera chaka chatha pomwe malemuwa adalowa m’manda.

A Zonyera Zambuzi awalonga ufumu kutsatira pomwe Inkosi Ya Makosi Gomani V, inavomereza dzina la a Zonyera Zambuzi kukhala mlowam’malo wa ufumu wa Kachindamoto.

Poyankhulapo pamwambowu, Nduna yoona zamaboma ang’ono, a Ben Malunga Phiri, alangiza Mafumu andodo m’bomali, kuti apewe kuyitanitsa ndalama kwa mafumu ang’onoang’ono omwe akufuna kuwakweza ufumu, zomwe anati ndizopereka chitsanzo choipa.

Zambuzi

A Phiri amayankhula izi pomwe amalangiza a Zonyera Zambuzi munthawi yomwe amawaveka mkanjo kukhala Senior Chief Kachindamoto VIII.

A Phiri anati a Zonyera Zambuzi atengere chitsanzo chabwino cha malemu Senior Chief Theresa Kachindamoto Vll.

Malinga ndi a Phiri, malemu Senior Chief Theresa Kachindamoto anakwanitsa kuthetsa maukwati a ana okwana 3,500 ndikuwonetsetsanso kuti ana akupita ku sukulu.

Apa mfumu yomwe inayimira Ngwenyama iNkosi Ya Makosi Gomani V, Senior Chief iNkosi Makwangwala alangiza mafumuwa kuti asamalande malo kwa anthu.

Mfumuyi inapitilira ndikumema anthu kuti azilemekeza mafumu awo.

Kupatula kulonga ufumu a Zonyera Zambuzi kukhala mlowam’malo wa ufumu wa Kachindamoto, mafumu enanso awakweza kukhala ma gulupu pamwambowu.

Did you enjoy this article?

Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.

Across the AtmosphereDiscussions