Scorchers yakodolera Flames chitozo
“Kodi sizingatheke kuti Flames ija adzikamenya atsikana athuwa?” “Flames ija angoithetsa kaye bwanji.” Izi ndi zina mwa ndemanga zomwe zatsikira m’masamba anchezo pomwe Scorchers yapumitsa a Malawi kumwa wa mandimu. Koma tadikirani kaye, katswiri wa timu ya Blue Eagles yemweso mwa apo ndi apo amatha kuitanidwa kukasewerera timu ya Flames, Micium Mhone, ali ndi uthenga...
Kodi sizingatheke kuti Flames ija adzikamenya atsikana athuwa?” “Flames ija angoithetsa kaye bwanji.” Izi ndi zina mwa ndemanga zomwe zatsikira m’masamba anchezo pomwe Scorchers yapumitsa a Malawi kumwa wa mandimu.
Koma tadikirani kaye, katswiri wa timu ya Blue Eagles yemweso mwa apo ndi apo amatha kuitanidwa kukasewerera timu ya Flames, Micium Mhone, ali ndi uthenga wanu: Akuti musaisambwadze timu ya madodayi.
Kuyambira pomwe timu ya atsikana ododa chikopa, The Scorchers yakhala ikuchita bwino ku mpikisano wa WAFCON m’dziko la Morocco, timu ya abambo, The Flames yakhala ikupumira m’mpanthi.
Anthu pa masamba amchezo akhala akuyiserewula Flames kuti kwa nthawi yaitali yawamwetsa anthu okonda mpira m’dziko muno mandimu.
“Flames ija mungoithetsa imationongera ndalama zathu ulele,” iyo idali ndemanga ya Florence Gondwe pa tsamba lathu la fesibuku potsatira chipambano cha Scorchers pomwe inkasewera ndi Nigeria ku ndime ya Magulu (group stages).
Ndemanga ngati izi zidafumbulaso Lamulungu lapitali pomwe Scorchers idagonjetsa Ghana 2-1 kuti idzugulire malo ku Semifinal ya WAFCON. Chipambano cha Lamulungu chapangitsaso Scorchers kudzigulira malo ku mpikisano wa FIFA World Cup chaka cha mawa.
Lachitatu lidaliso tsiku lina lomwe labweretsa chitozo ku timu ya Flames. Scorchers yagonjetsa Algeria 3-1 kuti idzipezere malo ku masewero omaliza achikhochi, zomwe zawinjezera chitozo pa timu ya abamboyi.
“Infact osewera onse a Flames akuyenera kumangidwa, ationongera misonkho yathu nthawi yaitali,” adatero Luciano Jiya Ngondo yemwe adaikira ndemanga pa tsamba lathu pa nkhani ya chipambano cha Scorchers.
Kupatula pa tsamba lathu, anthu ochuluka m’masamba ena, akuthera zakukhosi timu ya anyamata yadziko linoyi.
Koma mmodzi mwa osewera a Flames Micium Mhonde wadzudzula mchitidwewu ponena kuti chisangalalo chapano chisasanduke chitozo ku Flames.
“Tiyeni tisangalare koma tisanyoze ena,” Mhone wolemba pa tsamba lake la fesibuku komwe kwafika ndemanga ngati mchenga.
Flames idapitako ku mpikisano wa AFCON katatu; mu 1984, 2010 ndi mu 2021, koma maulendo onsewa siimafika patali ngati momwe Scorchers yachitira.
Potsatira chipambano cha Lachitatu, Scorchers yomwe yapita ku WAFCON koyamba, ikumana nd Cameroon Lamulungu lino pa masewero omaliza ampikisanowu.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.