Skip to content

A Malawi ambiri akunyerabe ku tchire

Ngakhale m'madera ambiri muli zikwangwani zoti “tidasiya kunyera ku tchire,” zadziwika kuti iri ndi bodza lankunkhuniza chabe pomwe lipoti latsindika kuti anthu ambiri alibe zimbudzi ndi zipangizo zina za ukhondo.Izi zadziwika Lachisanu pa mwambo wotsegulira Presidential Compact on Water, Sanitation and Hygiene (WASH), komwe Wachiwiri kwa Nduna ya Zaumoyo ndi Ukhondo, Charles Chilambula, adati dziko...

Malawi24
Aug 15, 20262 min read

gakhale m’madera ambiri muli zikwangwani zoti “tidasiya kunyera ku tchire,” zadziwika kuti iri ndi bodza lankunkhuniza chabe pomwe lipoti latsindika kuti anthu ambiri alibe zimbudzi ndi zipangizo zina za ukhondo.

Izi zadziwika Lachisanu pa mwambo wotsegulira Presidential Compact on Water, Sanitation and Hygiene (WASH), komwe Wachiwiri kwa Nduna ya Zaumoyo ndi Ukhondo, Charles Chilambula, adati dziko lino silikuchita bwino pa nkhani ya ukhondo.

Malingana ndi Chilambula, lipoti la kafukufuku wa Malawi Demographic and Health mchaka cha 2024, lasonyeza kuti m’madera akumidzi, anthu 40 okha pa 100 alionse ndiomwe ali ndi zimbudzi komaso zipangizo zina zolimbikitsira ukhondo.

Vutoli silinakhudze madera akumidzi okha pomwe Chilambula wati kafukufukuyu adasonyezaso kuti m’madera akutawuni, anthu 44 okha pa 100 alionse ndiomwe ali ndi malo oyenerera komaso zipangizo zoyenera zochitira ukhondo.

Iye anati vutoli silikukhudza m’makomo okha, koma ngakhaleso m’sukulu ndi m’zipatala, zomwe wati zikuyika anthu pachiwopsezo cha matenda osiyanasiyana komanso kuwonongeka kwa chilengedwe m’dziko muno.

“Pa chiwerengerochi pali ana omwe amapita kusukulu komwe kulibe malo ochitira ukhondo, komanso odwala ndi ogwira ntchito zaumoyo omwe amakhala m’zipatala momwe mulibe malo ochitira ukhondo okwanira,” adatero Chilambula.

Chilambula wapempha mabungwe ndi anthu onse m’dziko muno kuti agwirane manja polimbikitsa ntchito zokweza ukhondo, kuti dziko lino likwaniritse zolinga za ndondomeko yomwe yakhazikitsidwayi.

Iye anati boma likufuna kukweza chiwerengero cha anthu omwe ali ndi mwayi wopeza ntchito zaukhondo kuchoka pa 40 peresenti mu 2026 kufika pa 65 peresenti pofika chaka cha 2030.

Apa wachiwiri kwa ndunayu wati ndondomeko ya Presidential Compact on WASH ithandizira kuti lotoli likhale lotheka ndipo wati ndichitsimikizo cha kudzipereka kwa boma pa nkhani yokweza ukhondo m’dziko muno.

Did you enjoy this article?

Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.

Across the AtmosphereDiscussions