Boma laberedwa K700 miliyoni
Yemwe ankaona ngati boma siliberedwa, adali asanadziwe kuti kunja kuno kuli akathyali omwe atha kuinyenga kampani ya boma ngati National Oil Company of Malawi (NOCMA) Limited, mpaka iyo nkutumiza ndalama za nkhani nkhani za misonkho ya a Malawi ku akaunti yachinyengo.Pomwe inu mukamatumiza ndalama pa Airtel Money ndi TNM Mpamba mumayamba mwafusa kaye dzina la...
emwe ankaona ngati boma siliberedwa, adali asanadziwe kuti kunja kuno kuli akathyali omwe atha kuinyenga kampani ya boma ngati National Oil Company of Malawi (NOCMA) Limited, mpaka iyo nkutumiza ndalama za nkhani nkhani za misonkho ya a Malawi ku akaunti yachinyengo.
Pomwe inu mukamatumiza ndalama pa Airtel Money ndi TNM Mpamba mumayamba mwafusa kaye dzina la ejenti kapena munthu wolandirayo kuti mutsimikize ngati ndalama sizikupita kolakwika, NOCMA zimenezo inalibe nazo ntchito, koma pano manja ali mkhosi pomwe yayeretsedwa m’maso.
Akatswiri a kompyuta omwe sakudziwika, adanyenga NOCMA kuti itumize ndalama zokwana US$403,605, yomwe ndi yopitirira K700 million ku akaunti yachinyengo, podziyerekeza kuti ndi kampani ya Mozhandling Limited, kampani ya ku Mozambique yomwe imayang’anira mafuta pa doko la Nacala.
Malipoti akusonyeza kuti akathyaliwa adalanda maimelo a Mozhandling Limited, kenako adadziyerekezera ngati kampaniyo n’kupereka nambala yabodza ya akaunti yakubank.
Atsizinantolewa adauza NOCMA kuti Mozhandling yatsegula akaunti yatsopano ku Bank of America, zomwe NOCMA inakhulupirira, ndipo pa 29 April 2026 inalamula National Bank of Malawi kutumiza ndalamazo.
Patadutsa milungu iwiri, ndipomwe NOCMA idazindikira kuti yachanutsidwa, pomwe woimira Mozhandling weniweni adalumikizana ndi NOCMA kufunsa za ndalama zomwe kampaniyo inkayembekezera.
NOCMA yati pano Malawi Police Service komaso Bank of America ayamba kufufuza kuti apeze komwe ndalamazo zapita.
Padakali pano, anthu ambiri akufusa ngati NOCMA inatsatiradi ndondomeko zonse zoyenera isanatumize ndalama za nkhani nkhani za misonkho ya a Malawi’zi.
Anthu ena akuti ngati bungwe lomwe limayang’anira ndalama za misonkho ya a Malawi, NOCMA imayenera kutsimikiza kaye ngati akauntiyo inalidi ya Mozhandling Limited isanatumize ndalamazi.
Izi zikudza pomwe boma mu 2022 lidalipira US$727,000 yomwe idala K750 miliyoni nthawi imeneyo ku kampani yogulitsa nyama ya Barkaat Foods Limited, m’dziko la United Kingdom, pofuna kugula feteleza wa mundondomeko ya Affordable Inputs Programme (AIP).
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.