Chisale wapeleka galimoto zinayi
Anthu okhala m'dera la Champiti m’boma la Ntcheu atola khasu ndi mpini omwe pomwe phungu wawo Norman Chisale wawadalitsa ndi galimoto zinayi.Ziwiri mwa galimotozi ndi zonyamula odwala (ambulasi), pomwe ziwiri zinazo ndi zikuluzikulu zonyamula katundu osiyanasiyana.Polankhula Loweruka pamwambo wopereka galimotozi pabwalo la sukulu ya pulaimale ya Champiti, Chisale wati wachita izi pofuna kuthana ndi mavuto...
nthu okhala m’dera la Champiti m’boma la Ntcheu atola khasu ndi mpini omwe pomwe phungu wawo Norman Chisale wawadalitsa ndi galimoto zinayi.
Ziwiri mwa galimotozi ndi zonyamula odwala (ambulasi), pomwe ziwiri zinazo ndi zikuluzikulu zonyamula katundu osiyanasiyana.
Polankhula Loweruka pamwambo wopereka galimotozi pabwalo la sukulu ya pulaimale ya Champiti, Chisale wati wachita izi pofuna kuthana ndi mavuto a mayendedwe kwa odwala akafuna kukapeza thandizo lachipatala komaso pofuna kupititsa ntchito zachitukuko patsogolo.
Malingana ndi a Chisale yemwenso ndi wachiwiri kwa nduna yoona za chitetezo cha m’dziko, galimotozi zizinyamula odwala omwe atumidzidwa kukalandira thandizo lamankhwala kuchipatala cha Ntcheu ndi zipatala zina.
Phunguyu wachenjeza kuti pasapezeke aliyense wolowetsa ndale pa galimotozi ponena kuti zaperekedwa kutumikira wina aliyense kuderali.
Poyikira ndemanga za mphatsozi, mfumu Champiti yayamikira thandizoli lomwe ati labwera munthawi yake.
Mfumuyi yati anthu amderali amakumana ndi mavuto osiyanasiyana okhudza mayendedwe maka pofuna kukapeza thandizo ku chipatala cha Ntcheu.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.