Skip to content

Tsoka likalimba: Wanderers ikusakabe ‘Pin’ ya Airtel Money

Imaona ngati idutsa mofewa poti m'daniyo ndi mwana wa m'nyunba, koma mhuu! Mwamuna nzako mpachulu. Mighty Wanderers ikupitilira kulakwitsa nambala ya chinsinsi kuti itape khusa pa ejenti wa Airtel Money. Lamulungu, panali nkhondo ya pa chiweniweni pa bwalo lla Bingu munzinda wa Lilongwe, pomwe Ekhaya yomwe imatsogolereredwa ndi William Mpinganjira, yagonjetsa Manoma yomwe imathandizidwa ndibambo...

Malawi24
Aug 30, 20261 min read

maona ngati idutsa mofewa poti m’daniyo ndi mwana wa m’nyunba, koma mhuu! Mwamuna nzako mpachulu. Mighty Wanderers ikupitilira kulakwitsa nambala ya chinsinsi kuti itape khusa pa ejenti wa Airtel Money.

Lamulungu, panali nkhondo ya pa chiweniweni pa bwalo lla Bingu munzinda wa Lilongwe, pomwe Ekhaya yomwe imatsogolereredwa ndi William Mpinganjira, yagonjetsa Manoma yomwe imathandizidwa ndibambo ake, Thomson Mpinganjira 2-1.

Zigoli za Blessings Malinda pa mphindi ya 38 kudzera pa penate ndi china cha Allen Chihana, zinali zokwanira kuti Ekhaya ipochere 40 million kwacha pa ejenti wa Airtel Money.

Mbali inayi, Nyerere zinapata chigoli chopukutira misonzi kudzera mwa Mphatso Kamanga pa mphindi ya chitatu mchigawo cha chiwiri. Mtsogoleri wa timu ya Ekhaya William wati timu yake ya Ekhaya yazepula Wanderers chifukwa inalowa dala yokha mu ndime yotsiriza ya Airtel Top8.

William wayamika makolo ake kuti anawaphunzitsa bwino ana awo zokhudza kukonda Mpira ndi chifukwa chake lero akwanitsa kugonjetsa timu ya tate.

Iye wati sakanapangira mwina poti timuyi inalowa dala yokha mu mndime yotsiriza ya zamadolo Airtel Top8 season 9.

Did you enjoy this article?

Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.

Across the AtmosphereDiscussions