Chirango kwa bambo yemwe DNA yati mwana ndi wako
Akuluakulu a chipembedzo cha Chisilamu ati mwamuna yemwe wapita kukayezetsa DNA ndipo zotsatira zawonetsa kuti mwanayo ndi wake, akuyenera kulandira chirango. Izi ndi malingana ndi a Muhammad Uthman omwe ndi a Grand Mufti a m’dziko lino ku chipembedzochi, omwe ati mwamuna otere adzirangidwa chifukwa chokayikira komanso kunamizira mkazi wake kuti wachita chigololo.Iwo amayankhula izi mu...
kuluakulu a chipembedzo cha Chisilamu ati mwamuna yemwe wapita kukayezetsa DNA ndipo zotsatira zawonetsa kuti mwanayo ndi wake, akuyenera kulandira chirango.
Izi ndi malingana ndi a Muhammad Uthman omwe ndi a Grand Mufti a m’dziko lino ku chipembedzochi, omwe ati mwamuna otere adzirangidwa chifukwa chokayikira komanso kunamizira mkazi wake kuti wachita chigololo.
Iwo amayankhula izi mu pulogalamu ya mafunso ndi mayankho pa wayilesi ya Radio Islam.
Malinga ndi Uthman, ngati mwamuna ndi mkazi ali pa banja ndipo abereka mwana, koma bamboyo akufuna DNA chifukwa chokayikira kuti mkaziyo wachita zosayenera, amakhala akumunamizira mkaziyo kuti wachita chigololo.
A Uthman anati DNA imagwiritsidwa ntchito pofuna kutsimikizira umwini wa chinthu komanso ubale wa munthu ndi mwana.
Uthman anati zimenezi zili ndi chilango malinga ndi ziphunzitso za Chisilamu.
Iwo alimbikitsa Asilamu kuti azichita zinthu ndi umboni okwanira komanso kuopa Allah, kuti asadzapezeke kuti akulipira zoipa pa tsiku la Chiweruzo chifukwa cha kunamizira ena.
Malinga ndi Uthman, Qur’an komanso Hadith zimachenjeza anthu kuti asamanamize anzawo, makamaka pa nkhani ya chiwerewere, popanda kukhala ndi umboni wokwanira.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.