Rodwell athawira ku China nasiya a Malawi nalira
…”ndati ndikubwera”Mwambi woti ntchentche yotengeka imapsinjidwa ndi… lero waphelezera pomwe likukumwe la a Malawi omwe adagula malo ku kampani ya Rodwell Lumbe, pano manja ali mkhosi pomwe mkuluyu waboola mtambo, ndipo akuusumana ku China.Chatsitsa dzaye nchakuti anthu ena omwe adagula malo ku kampani yogulitsa malo ya Citizen Real Estate, ayeletsedwa m'maso pomwe akuti ena mwaiwo...
”ndati ndikubwera”
Mwambi woti ntchentche yotengeka imapsinjidwa ndi… lero waphelezera pomwe likukumwe la a Malawi omwe adagula malo ku kampani ya Rodwell Lumbe, pano manja ali mkhosi pomwe mkuluyu waboola mtambo, ndipo akuusumana ku China.
Chatsitsa dzaye nchakuti anthu ena omwe adagula malo ku kampani yogulitsa malo ya Citizen Real Estate, ayeletsedwa m’maso pomwe akuti ena mwaiwo sadapatsidwebe malo awo ngakhale kuti adapereka kale ndalama.
Malipoti akusonyeza kuti ena mwa anthuwa akamang’ala za nkhaniyi ku polisi ndipo ena akalanda katundu wa mu ofesi ya kampaniyi pofuna kuti abwezeredwe ndalama zawo.
Izi zikupherezera pomwe m’masamba anchezo kuyambira sabata yatha mwakhala mukuyenda chikalata chosonyeza kuti mwini kampaniyi, Lumbe akufunidwa.
Lumbe pokhala mwini filimu, akuganiziridwa kuti adapomboneza makasitomala ena posawapatsa malo awo ngakhale kuti adali atapereka kale ndalama.
Pomwe ena amaona ngati izi ndi tchetera chabe, lachiwiri, Lumbe wavomereza kuti padachitikadi misiteki, pomwe watsimikiza kuti anthu ena sadapatsidwe malo ngakhale adapereka kale ndalama za malowo.
“Kuyambira sabata ino, kampani iyamba kulumikizana ndi kasitomala aliyense payekhapayekha kuti tiwapatse malo awo,” watelo Lumbe muuthenga omwe analemba pa tsamba lakela fesibuku. “Aliyense amene sanalandirebe zikalata za malo ake apatsidwa zikalatazo potsatira ndondomekoyi.”
Kuwonjezera apo, Lumbe wavomereza kuti ma ofesi a kampaniyi atsekedwa kaye kaamba ka nkhanizi.
Lumbe watsimikizaso kuti pano ali m’dziko la China. Komabe, iye wati ulendowu sikuthawa makasitomala omwe wawachanutsawa.
“Masabata angapo apitawa, ndinapita ku Guangdong, China, kukachita nawo pulogalamu ya Community of Impact Leadership Programme. Iyi ndi pulogalamu yophunzitsa ndi kukulitsa luso la utsogoleri yomwe imatenga miyezi inayi,” wateloso Lumbe.
Izi zikutanthauza kuti kwa miyezi inayi a Malawi okhudzidwa akhaka akumudikirira Lumbe ngati mpulumutsi wolonjezedwayo kuti adziwe tsogolo la chuma chawo.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.