Skip to content

Mulungu musamumvere Mwanamvekha — Muluzi

Mtsogoleri wachipani chotsutsa cha UDF, Atupele Muluzi wapempha Mulungu kuti asavere zomwe yanena nduna yazachuma a Joseph Mwanamvekha, kuti onyoza utsogoleri wa a Arthur Peter Mutharika adzifa. Muluzi walemba izi pa tsamba lake la Facebook, pomweso wayika kanema wowonetsa a Mwanamvekha akuyankhula ku Mulhako Wa Alhomwe, komwe amadzudzula anthu ena omwe akuti akuchita motsutsana ndi...

Malawi24
Oct 19, 20262 min read

tsogoleri wachipani chotsutsa cha UDF, Atupele Muluzi wapempha Mulungu kuti asavere zomwe yanena nduna yazachuma a Joseph Mwanamvekha, kuti onyoza utsogoleri wa a Arthur Peter Mutharika adzifa.

Muluzi walemba izi pa tsamba lake la Facebook, pomweso wayika kanema wowonetsa a Mwanamvekha akuyankhula ku Mulhako Wa Alhomwe, komwe amadzudzula anthu ena omwe akuti akuchita motsutsana ndi a Mutharika.

A Mwanamvekha anati ndiokhumudwa kuti anthu ena omwe sankadziwika isanafike 2014, ndipo Mutharika anawaika m’maudindo, pano ayamba kumutukwana mtsogoleri wa dzikooyu.

Iwo anachenjeza, pogwiritsa ntchito vesi yamu baibulo kuti omwe akuchita mosemphana ndi a Mutharika afe ndithu.

“Ndie tiyang’ane pa Eksodo 21 vesi ya 17 pomwe akuti onyoza akulu akuyenera afe ndithu” anatero a Mwanamvekha.

Iwo anapitiriza kunena kuti atumidwa ndi a Mutharika kuti akuwona anthu onse omwe akufuna udindo wawo ndipo anati enaso anayesera kupanga zotere mbuyomo koma lero ndi anthu wamba.

Koma izi sizinamveke bwino kwa a Muluzi omwe anapempha Mulungu kuti alowererepo posalola kukwanilitsidwa kwa mawu a Mwanamvekha kuti aliyese wodzudzula kusayendetsa bwino kwa dziko afe.

“Chifukwa chani aliyese oyankhula zovuta za utsogoleri adzifa? Tikuchikana mu mdzina la Mulungu kuti chilichonse chomwe chanenedwa chisachitike,” atero a Muluzi.

Izi zikudza pomwe pali mtsutso waukulu pomwe akuluakulu ena aboma akhala akutsutsana ndi ganizo la sipikala wa nyumba yamalamulo kuti pakhale kafukufuku wa katangale m’boma.

Kuphatikiza apo, pakhalaso manong’onong’o akagwiridwe ka ntchito ka wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Jane Ansah kuti sakupatsidwa mpata.

Did you enjoy this article?

Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.

Across the AtmosphereDiscussions