Skip to content

Joe Ikon avulala atadziponya pa siteji

Mawu woti timba anathyoka mwendo dansi yothaitha aphelezela pa woyimba Joe Ikon yemwe wavulala atichita ukandiyerekere pagulu podziponya pa nsanja. Woyimbayu anali ndi phwando la mayimbidwe Loweruka munzinda wa Blantyre lomwe amalitcha kuti “Mwana wa Atate” komwe khwimbi linasonkhana. Kamena wina yemwe akuzungulila pa masamba amchezo, akuonesa Ikon akuchoka pa nsanja ndikudziponya ku malo omwe...

Malawi24
Oct 25, 20261 min read

awu woti timba anathyoka mwendo dansi yothaitha aphelezela pa woyimba Joe Ikon yemwe wavulala atichita ukandiyerekere pagulu podziponya pa nsanja.

Woyimbayu anali ndi phwando la mayimbidwe Loweruka munzinda wa Blantyre lomwe amalitcha kuti “Mwana wa Atate” komwe khwimbi linasonkhana.

Kamena wina yemwe akuzungulila pa masamba amchezo, akuonesa Ikon akuchoka pa nsanja ndikudziponya ku malo omwe kunali anthu.

Ngakhale zili choncho, sizikudziwika ngati woyimbayu anavulala podupha kapena ngati wavulala kamba koti anafikira pansi atadumpha.

Pakadali pano, woyimbayu wayika pa tsamba lake la fesibuku chithunzi chowonetsa mwendo omwe wavulala utakutidwa ndi nsalu zakuchipatala.

Komabe, Ikon sanafotokoze kuti wavulala motani koma wangolemba mawu omwe akusonyeza kuti pano akunong’oneza bondo pa zomwe anachitazo.

“Dzulo tinasangalala kwambili khalangati,” walemba choncho Ikon.


.

Did you enjoy this article?

Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.

Across the AtmosphereDiscussions