Zipembedzo m’dziko muno zimaloleza kuchotsa mimba
Ngakhale kwa nthawi yayitali pakhala mtsutso pa malamulo a dziko lino komaso a zipembedzo ngati n'koyenera kuti amai ndi atsikana adzichotsa mimba, kafukufuku wapeza kuti dziko lino komaso mipingo izi ndizololedwa.Izi zadziwika lachiwiri pa maphunziro omwe bungwe lopereka ntchito zokhudza umoyo wa uchembere, kulera, komanso zaumoyo wa amayi ndi ana, la Banja la Mtsogolo linakonzera...
gakhale kwa nthawi yayitali pakhala mtsutso pa malamulo a dziko lino komaso a zipembedzo ngati n’koyenera kuti amai ndi atsikana adzichotsa mimba, kafukufuku wapeza kuti dziko lino komaso mipingo izi ndizololedwa.
Izi zadziwika lachiwiri pa maphunziro omwe bungwe lopereka ntchito zokhudza umoyo wa uchembere, kulera, komanso zaumoyo wa amayi ndi ana, la Banja la Mtsogolo linakonzera magulu osiyanasiyana okhudzidwa munzinda wa Lilongwe.
Mmodzi mwa anthu omwe anali nawo pa maphunzirowa, Kenneth Mtago omwe ndi mkulu wa bungwe la Young Voices anati ngakhale zipembedzo zambiri sizibwera poyera kuloleza kuchotsa pakati koma zimapereka danga kwa anthu awo kutero.
“Zipembedzo zikuluzikulu m’dziko muno ngati katolika, chisilamu, CCAP, Seventh Day ngakhale zimaletsa kuti anthu awo adzichotsa pakati koma zimapereka danga lotero pokhapokha ngati moyo wamunthu uli pachiwopsezo chifukwa zipembedzo zonsezi zimanena kuti ndikwabwino kupulumutsa miyoyo,” anatero Mtago.
Iwo anapitiriza ndi kukumbutsa anthu kuti malamulo a dziko lino amaperekaso mwayi kwa amayi ndi atsikana kuchotsa pakati, koma anatsindika kuti si aliyese amayenera kupanga izi.
“Malamulo adziko lino akuloleza atsikana osadutsa zaka 18 komaso amayi omwe miyoyo yawo ili pachiwopsezo kuchotsa pakati kutanthauza kuti amayi ndi atsikana mdziko muno ali ndi ufulu ochotsa mimba ngati akuwona kuti ndikoyenera”.
Mtago anapitiriza kunena kuti mwayi ochotsa mimba umadutsa m’ndondomeko zingapo kuphatikizapo kupita ku polisi kukatenga lipoti losonyeza kuti munthu wagwiriridwa ndipo akuyenera kupatsidwa danga lochotsa pakati ngati wafuna.
Malingana ndi a Mtago, kusapatsidwa mwayi kwa amayi ndi atsikana kuchotsa pakati kamba ka chipembedzo ndizikhulupiro, kukupangitsa amayi apakati pa 8 mpaka 18 pa 100 aliwose kumataya miyoyo kamba kochotsa mimba mu njira zosayanera.
Pa mkumanowu, anakambiranaso nkhani zokhudza uchembere wabwino ndi ufulu wa amayi okapimidwa ndi kutsimikiza ngati mimba yachoka yokha.
M’mau ake, katswiri wa zamalamulo woyimira bungwe la Banja la Mtsogolo, Zaithwa Milanzi anati pali zinthu zambiri zomwe anthu samadziwa pofuna kuteteza miyoyo monga ufulu wa atsikana osapyola zaka 18, kuchotsa pathupi ngati nkoyenera kutero.
Apa iwo alangiza anthu kuti ngakhale ali ndi zikhulupiro m’zipembedzo zawo, sakuyenera kunyalanyaza malamulo oyendetsera dziko lino.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.