Wogulitsa nyama ya galu wayithyola mukhothi
Njonda yomwe ikuyankha mlandu ogulitsa nyama ya galu ku Kasungu, inayithola m'maso muli gwa mukhothi pomwe inati inapha galuyo osati kuti igulitse.Juma Sabiano wa zaka 49, wam'mudzi mwa Chisinga m’bomali, wamayankhula izi podzitetezera pa mlanduwu pamene amaonekera ka chiwiri ku bwalo la mirandu. Sabiano ndi mzawo Chisomo Willard adanjatwa mwezi wa June m'mudzi mwa Chisinga...
jonda yomwe ikuyankha mlandu ogulitsa nyama ya galu ku Kasungu, inayithola m’maso muli gwa mukhothi pomwe inati inapha galuyo osati kuti igulitse.
Juma Sabiano wa zaka 49, wam’mudzi mwa Chisinga m’bomali, wamayankhula izi podzitetezera pa mlanduwu pamene amaonekera ka chiwiri ku bwalo la mirandu.
Sabiano ndi mzawo Chisomo Willard adanjatwa mwezi wa June m’mudzi mwa Chisinga powaganizira kuti amagulitsa nyama ya galu.
Ataonekera kubwali koyamba, iwo adaukana mlanduwu, zomwe zidapangitsa Chief Resident Magistrate Brian Sambo kuwuza mbali yaboma kubweretsa mboni pa nkhaniyi.
Ataonekeranso kubwaloli a Sabiano anauza bwaloli kuti anapha galuyo ngati ndiwo yapakhomo osati yogulitsa.
Apa bwaloli layika tsiku la pa 12 August mwezi wamawa ngati tsiku lomwe lidzapereke chigamulo chake.
A Sabiano amachokera m’mudzi mwa Chiuta m’boma la Chiladzulu.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.