Skip to content

Bambo wagamulidwa pogulitsa malonda malo olakwika

Kugulitsa apozi pa Nandozi munzinda wa Blantyre kwalanga bambo wina yemwe khothi lamugamula kuti apereke chindapusa, apo bii akalowe kumpanda.Bwalo la mirandu la Magistrate mu mzinda wa Blantyre lagamula Lawrence James kupereka chindapusa cha K20,000 kapena kukaseweza jere kwa miyezi 12, kaamba kopezeka akugulitsa apozi (apples) malo osayenera.A Kingsley Matope, omwe ndi oyimira boma pa...

Malawi24
Jul 31, 20261 min read

ugulitsa apozi pa Nandozi munzinda wa Blantyre kwalanga bambo wina yemwe khothi lamugamula kuti apereke chindapusa, apo bii akalowe kumpanda.

Bwalo la mirandu la Magistrate mu mzinda wa Blantyre lagamula Lawrence James kupereka chindapusa cha K20,000 kapena kukaseweza jere kwa miyezi 12, kaamba kopezeka akugulitsa apozi (apples) malo osayenera.

A Kingsley Matope, omwe ndi oyimira boma pa mlanduwu adauza khothi Lachinayi kuti, a James adapalamula mlanduwu Lachiwiri pa 28 July 2026, pafupi ndi pa Nandozi munzindawu.

Matope wati James adagwidwa ndi ogwira ntchito ku khonsolo ya mzinda wa Blantyre omwe amayendera madera ena a mzindawu.

Ogwira ntchito ku khonsolowa, amayendera mzindawu pofuna kuona ngati anthu akutsatira malamulo okhudza malo ochitira malonda, komwe anapeza James akugulitsa apozi malo osaloledwa.

Atawonekera ku bwalo la milandu, James adavomera mlanduwu koma adapempha bwaloli kuti limukhululukire ponena kuti ali ndi banja lomwe limadalira iye komanso ndalama yomwe amachitira malonda ndiyangongole.

Apa bwaloli lidagamula kuti mkuluyu apereke K20,000 kapena akagwira ntchito ya kalavula gaga kwa chaka chimodzi. James adawonetsa chidwi chopereka ndalamayi kuti asakaseweze jere.

James ndiwochokera m’mudzi wa Maliyera mdera la mfumu yaikulu Mabuka m’boma la Mulanje.

Did you enjoy this article?

Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.

Across the AtmosphereDiscussions