Wanjinga wafa pothawitsa mafuta kwa apolisi
Woyendetsa njinga yamoto yemwe ananyamula zigubu zamafuta a galimoto, wafa atagwa ndikuyaka moto pomwe amathamangitsidwa ndi a polisi. Malingana ndi yemwe tawona pa tsamba la Facebook, izi zachitika pa Kanengo mu mzinda wa Lilongwe. Mu kanemayu mukuveka mau a yemwe amajambula ndipo wafotokoza kuti wanjingayu amathawa galimoto yapolisi yomwe imamuthangitsa, koma anakagwera kutchire komwe moto...
oyendetsa njinga yamoto yemwe ananyamula zigubu zamafuta a galimoto, wafa atagwa ndikuyaka moto pomwe amathamangitsidwa ndi a polisi.
Malingana ndi yemwe tawona pa tsamba la Facebook, izi zachitika pa Kanengo mu mzinda wa Lilongwe.
Mu kanemayu mukuveka mau a yemwe amajambula ndipo wafotokoza kuti wanjingayu amathawa galimoto yapolisi yomwe imamuthangitsa, koma anakagwera kutchire komwe moto unabuka.
“Pothawa a polisi, wakagwera kutchire ndipo njinga yayaka ndi munthu yemweyo wafera pomwepo,” anatero wojambulayu.
Iye wati a polisi atawona izi sanayime pamalopa angozipo ndipo pomwe anthu amafikapo moto unali utakolera kwambiri.
Izi zikudza pomwe mafuta akhala akuvuta kwambiri m’dziko, zomwe zapangitsa anthu ena kumagulitsa pa msika osavomerezeka.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.