Tikupwetekani — Mpuluka waopseza andale
…wati agwiritsa ntchito mtera …nawo onyoza Mutharika achenjezedwa Mukumanyoza m’tsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika? Samalani. Ku mwambo wa Mulhako wa Alhomwe wa chaka chino kwatuluka chenjezo lomwe akuti ngati sizisintha mutha nonse psiti! Apo bii kum’mwera mukuvera fungo. Wapampando wa Mulhakho wa Alhomwe, Muchanakwaye Mpuluka, wachenjeza anthu onse omwe akumasokoneza chikhalidwe cha Chihlomwe komanso...
…wati agwiritsa ntchito mtera
…nawo onyoza Mutharika achenjezedwa
Mukumanyoza m’tsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika? Samalani. Ku mwambo wa Mulhako wa Alhomwe wa chaka chino kwatuluka chenjezo lomwe akuti ngati sizisintha mutha nonse psiti! Apo bii kum’mwera mukuvera fungo.
Wapampando wa Mulhakho wa Alhomwe, Muchanakwaye Mpuluka, wachenjeza anthu onse omwe akumasokoneza chikhalidwe cha Chihlomwe komanso onse omwe akumanyoza mtsogoleri wa dziko lino kuti awona mbonawona.
Poyankhula Lamulungu pa mwambo wa chaka chino kwa Chonde m’boma la Mulanje, Mpuluka wati gulu lawo ndilokhumudwa kuti anthu ena andale akufuna kumaipitsa mbiri ya anthu a mtundu wa Chilhomwe.
“Izi ndikuyankhula chifukwa tatopa. Alhomwe Ali apawa ndiomwe amavutika nthawi ndi nthawi nde lero chifukwa choti awiri atatu apeza suku akudya mukunena kuti Alhomwe tonse tikudya. Tatopa nanu, takukwiyirani musazayambireso tikupwetekani,” watero Mpuluka.
Mpuluka wadzudzulaso anthu onse omwe akunyoza m’tsogoleri the dziko lino, Mutharika. Apa iwo awopseza kuti athana ndi onse omwe angapitirize kumatukwana mtsogoleriyu yemweso ndi tate wa gulu la Mulhako wa Alhomwe.
“Ife Alhomwe sitimasangalala mukamatitukwanira patron wathu. Muuzane ife kuno munthu akatukwana patron wathu sitimamukhululukira. Kundaleko mumakhululukirana koma ife kuno ayi.
“Tikangokuonani kuti mwatukwana patron wathu kaya uko mumamuti president izo ndi zanu, ife sitikukhululukirani tithana nanuso,” watelo Mpuluka.
Mpuluka anapitirira kutambasula za momwe athanirane ndionse omwe akusokoneza gulu la Mulhako wa Alhomwe komanso omwe akutukwana a Mutharika, ponena kuti agwiritsa ntchito njira ziwiri.
“Kuwamaliza komwe tingawamalize tigwiritsa ntchito mankhwala. Kachiwiri sadzalowaso kwathu kuno, physical, “ wateloso Mpuluka.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.