Skip to content

Alipo anthu amene anawononga zinthu koma savomereza – Kunkuyu

Mkulu woona zokopa anthu mu chipani cha Malawi Congress Party (MCP), a Moses kunkuyu ati ndikofunika kuyamikila m’tsogoleri wakale, a Lazarus Chakwera Kamba koti amabwera poyera ndikuyankhula kuti pali magawo ena omwe sanayendetse bwino pamene anali m’boma. Iwo ati alipo anthu ena amene anawononga zinthu koma samakhala ndi mtima ofuna kubwera pa maso pa a...

Malawi24
Nov 5, 20262 min read

kulu woona zokopa anthu mu chipani cha Malawi Congress Party (MCP), a Moses kunkuyu ati ndikofunika kuyamikila m’tsogoleri wakale, a Lazarus Chakwera Kamba koti amabwera poyera ndikuyankhula kuti pali magawo ena omwe sanayendetse bwino pamene anali m’boma.

Iwo ati alipo anthu ena amene anawononga zinthu koma samakhala ndi mtima ofuna kubwera pa maso pa a Malawi ndikuzafotokoza kuti pakuti sizinayende bwino.

Iwo anena izi potengera kuti m’tsogoleri wa chipani a Lazarus chakwera akhala akuyankhula m’mikumano ya chipanichi kuti anthu ena amati akawatuma amakapanga zinthu zina zosiyana ndizomwe atumidwa.

A Kunkuyu amayankhula izi pamene amacheza ndi tsamba lina lowulutsa mawu la LAB20 podcast mu pulogalamu ya the hot seat.

Iwo adati ndi zinthu zabwino popeza kuti a Chakwera amavomeleza zina mwa zinthu zomwe zinavuta, chifukwa nkutheka anthu pamene amakhala kumanena za nkhani yokhuza ulamuliro wawo pali zinthu zina zomwe sanawanenele bwino kapena kufotokoza zonse zonkhuza nkhaniyo.

“ngati akubwera kuti pakuti sitidatere, pakuti tidatere, tiyeni titenge chimenecho kuti pa mawa tizakumbukile kuti kunali President wa dziko, anali president wa Malawi Congress Party ndipo nthawi inayake adazichepetsa nkuzatiuza kuti pakuti sizinakhale bwino,” Adatero Kunkuyu

Kunkuyu anayankhulaso pa nkhani yokhudza kuyimitsidwa kwa nkumano wa a phungu a ku nyumba ya malamulo.

Iwo adati izi zitachitika anali okhumudwa kwambili chifukwa nkumano wa aphungu akunyumba ya Malamulo cholinga chake ndikukambirana za udindo umene aphunguwa alinawo potumikila anthu akudera komanso a Malawi.

Did you enjoy this article?

Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.

Across the AtmosphereDiscussions